Langwan Piksy - Pakati lyrics

Published

0 85 0

Langwan Piksy - Pakati lyrics

VERSE ONE Pakati, pa kuwala ndi mdima Pakati, pakutentha ndi kuzizira Pakati, pa chubu ndi mpira Pakati, pa nkhuku ndi dzira Nkakhala ofunda mudzandilavula Sinfuna kulavulidwa Sinfuna kulavulidwa Ndiri ngati munda wosalambula Ndifuna kupaliridwa Ndifuna kupaliridwa CHORUS Mundiike kumene mufuna Mundiike kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inu Mundiike kumene mufuna Mundiike kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inuyo VERSE TWO Pakati, pa mbuzi ndi gwape Pakati, pa galu ndi nkhadwe Pakati, pa dzulo ndi lero Pakati, pa usiwa ndi ulemelero Nkakhala ofunda mudzandilavula Sinfuna kulavulidwa Sinfuna kulavulidwa Ndiri ngati munda wosalambula Ndifuna kupaliridwa Ndifuna kupaliridwa CHORUS Mundiike kumene mufuna Kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inu Kumene mufuna Mundiike kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inuyo VERSE THREE Sindziwa za mawa Tsono ndikhala ndi nkhawa Ndikhala moyo wa mantha Njira yanga iwunikidwe Odziwa za ku mwamba Akuti ndiri nziwanda Ndikhala moyo wa mantha Ndingatani ndimasulidwe Ndingatani ndimasulidwe Ndiri pa katiiii CHORUS Mundiike kumene mufuna Kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inu Kumene mufuna Mundiike kumene mufuna Kuti zonse zomwe ndichita Zisangalatse inuyo