Langwan Piksy - Mthunzi lyrics

Published

0 343 0

Langwan Piksy - Mthunzi lyrics

CHORUS Ndikufuna mthunziwo Sindufuna Nkhunizo Chonde musadule Mtengo wangawo Nthawi zina sitikamba zofunika kukambidwa Sitikankha zofunika kukankhidwa Pena Sitikanda pofunika kukandidwa Dziko linasintha timaopa kutayidwa Ma born again Sangacheze nawe unless you born again But then again Ndingasinthe bwanji ngati muku leader life ngati muli kumwamba kale U seem so far away Yesu anadzera ochimwa Miyala yokanidwayo These days ndiimene ikusalidwayo Think again If you really born again Njira yanuyo tilondolereni CHORUS Ndikufuna mthunziwo Sindufuna Nkhunizo Chonde musadule Mtengo wangawo Abambo prophet akazi awo prophetess Chondidabwitsa amakhala ndi confidence Ine I thought zimayendera maitanidwe Mesa ndimphatso Yoti ena alibe Pa banja panu mwayambisa yanu church Dzina lake pa Google mwachita search Tilibe mphavu zokupangirani judge Koma ngati nku jahena chonde msatipange drag Kuuza anthu amu mpingo mwanu alemera Akhristu anu kupusa amayamba kusekelera Amen! Mulungu achita kothekera Kusiya kulimbikira ntchito nkumangopemphera Kenako amayamba nsanje Mwawasocheretsa Kukhulupira ulosi wanu mwawasokoneza Awa nga satanic Awa kukhwima chabe awa Neba wachikunja walemera mtima ukuwawa CHORUS Ndikufuna mthunziwo Sindufuna Nkhunizo Chonde musadule Mtengo wangawo Mutiuze za kumwamba Osati kumangotikomedwetsa nzapadziko pano Pano Muzinthu zonse, zonse zonse Ambuye akhalemo Amatero malembo Upindulanji ndi za mdziko ukutaya moyo wako? Musachulutse zokamba kuti tidzikuopani Tidzikweza Mulungu osati tidzikupopani Tidziona umulungu tikamakuonani Sing along to the song Muzinthu zonse, zonse, zonse Muzinthu zonse Ambuye akhalemo CHORUS Ndikufuna mthunziwo Sindufuna Nkhunizo Chonde musadule Mtengo wangawo